Gwamba “wadzibaya”
Yemwe adabweretsa mwambi woti kunena kwa ndithe ndithe nanthambwe adadzitengera, adalinga ataona kuti tsiku lina woyimba Duncan Zgambo, wotchuka ndi dzina loti Gwamba, adzadzilasa yekha pochita lonjezo losakwaniritsidwa.
Chatsitsa dzaye nchakuti pa 21 September, 2024, Gwamba yemwe omunyadira amamutcha GOAT, adali ndi mphwando la nyimbo pa bwalo la Civo munzinda wa Lilongwe lomwe ankalitcha “The Best of Gwamba Concert.”
Pa tsikuli kudali kubwira fumbi, pomwe oyimba ngati Focalistic wa m’dziko la South Africa komaso ena a pampanje pano, adadumphitsa anthu ma sipika.
Koma poti chuluke chuluke ndi wa njuchi umanena iyo yakulasa mbola, tsikuli linali la wamba makamaka kwa anthu okonda chamba, inde chamba cha lege poti utsi pa Civo sunafuke.
Gwamba sanaitane gulu la Black Missionaries, chomwe chinali chibwana cha mchombo lende. Ambiri okonda chamba cha lege sizidawakonde.
Patapita miyezi iwiri phwandoli chichitikireni, pa 5 November, 2024 Gwamba naye, adavomereza kuti kusatenga Ma Blacks idali “mistake” ndipo adalonjeza kuti sadzapangaso, mawu omwe lero amubwererera.
“Mkulu wanga! Ndamuuza kuti mistake yopanga show nkusiya ma Blacks sizachitikanso!! Ndasiya chibwana chimenecho,” adatelo Gwamba. “Ndakula ndasiya chibwana.”
Mawuwa amulasa woyimbayu kaamba koti phwando lotchedwa “Landlord Pa Kwawo” lomwe anachititsaso Loweruka lapitali pa bwalo la Bingu, kunalibe Ma Blacks.
Izi zapangitsa anthu kukafukula zomwe Gwamba adalemba pa 5 November, 2024 zija zolonjeza kuti sadzawasiyaso Ma Blacks, ndipo ambiri ati anali odabwa kuti gulu la chamba cha legeli silinaitanidweso.
“Ndiye apa simunawasiyaso. Palibwino kusiya onse aja ndikutenga ma blacks okha,” iyo idali ndemanga ya Ma Jamilah, yomwe siikusiyana ndi zomwe Chimzie Mmadih adalemba poti, “show ikhala bwanji yopanda ma blacks?”
Anthu ena akumbutsa woyimbayu kuti asamakomedwe polankhula. ” Osamatha mawu,” adatelo Achina Shame, pomwe Vitu Chisi adangoti, “nthawi mkachitsiru.”
Naye Elosie Mahau adakumbutsa “Landlord” kuti azikwanikitsa lonjezo ponena kuti intaneti siimaiwala munthu akalankhula.
Koma ngakhale zili choncho, anthu ena ati phwando la Loweruka linali kale bwino kotero Ma Blacks samafunikirako.
“Ma blacks achaniso m’mene zinaliri muja hhhh,” Violet Vionnah Violetta Kamwendo.
How it works
Once you click Generate, Ollama reads this article and crafts 5 comprehension questions. Your answers are graded against the article content — general knowledge won't be enough. Score 70+ to count toward your certificate.
Questions are cached — you'll always get the same 5 for this article.